Gospel Life
Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine
Sermons and teaching in Chichewa and English
Author
Gospel Life
Category
Podcast website
Latest episode
Apr 24, 2026
Where to listen?
Podcasts in the app Replaio Radio Coming soonPodcasts are coming to the app soon. Install now and be the first to see a whole new take on podcasts
Episodes
Mulungu ndi wabwino ndi wolungama/God is good and righteous 11.09.2023 51:08
Genesis 18:16-33 mulungu akuonetsera chilungamo chake pamene anthu akuchita zosutsana naye. Mulungu walinganiza zowononga Sodomu chifukwa cha uchimo wawo koma muzonsezi mulungu akukhalabe olungama. Chifukwa mulungu akuonetsera chilungamo chake mwa Abrahamu, zimene iyeyo ali ngati mulungu kuti iye amadalitsa komanso iye amawononga, iye amatembelera, iye amalanga. Mulungu waonetsera madalitso ake pa...
Khalani ophunzira weniweni wa Yesu Khristu/Be a true disciple of Jesus Christ 08.09.2023 41:52
Mateyu 5:1-3 ndime zamalemba izi ndi zofunika kwambiri kuwunikirana chifukwa ndi gawo limodzi la chiphunzitso chotchuka cha Yesu. Phunziro limene likupezeka mu ndime za malembazi ndi lakuti uthakukhala Nkhristu koma osakhala Nkhristu weniweni. Nkhani siyongopezeka ku malo opembedzera mulungu tsiku la mulungu kapena loweruka koma makamaka kukhala otsatira kapena ophunzira weniweni wa Yesu ngakhale...
Mulungu ndi odziwa zonse ndi wamphamvu/God is all knowing and all powerful 04.09.2023 44:21
Genesis 18:1-15 Kodi pali chimene ndi chokanika kwa mulungu? Akhristu nthawi zina timayetsedwa kuganiza kuti tili ndi kuthekera komuuza mulungu zomwe iye samadziwa. Koma kodi izi ndi zotheka? M'buku la Genesis 18 likutionetsera kuti mulungu ndi odziwa zonse ndi wamphamvu. Zonse zimene Abrahamu ndi Sara akudutsa ndi njira imene mulungu wayika kuti awiriwa amudziwe mulungu. Mulungu akudziwa pame...
Mulungu adalitsa Sara/God blesses Sarah 28.08.2023 46:25
Genesis 17:15-27, nthawi yayitali yadutsa Abrahamu wakula mopyola muyezo wobereka mwana ngakhalenso mkazi wake Sara. Mulungu akudalitsa Sara ndipo akuumuza Abrahamu kuti Sara azakhala ndi mwana yemwe azamutcha dzina lake Isake. Mulungu ndi wokhulupirika ndipo akusunga malonjezo ake. Izi zimaonekabe zosamvesetsa kwa Abrahamu chifukwa iye ndi mkazi wake anali atadutsa zaka zoberekera ana. Apa ndi pa...
Pangano la mdulidwe/Covenant Circumcision 21.08.2023 40:36
Genesis 17:1-14 mu pangano la mdulidwe mukupezeka zinthu zingapo zomwe ndi zofunika kuzimvetsetsa. Abusa a Hutchens akufotokozera bwino lomwe za pangano limeneli. Pangano la mdulidwe ndi mbali imodzi yotsindika kuti mbewu idzabwera kuchokera kwa Abrahamu. Izi zikugwirizananso ndi kusinthidwa dzina kwa Abram kukhala Abrahamu tate wa anthu ambiri. Mdulidwewu ulingati chidzindikiro chososnyeza kuti A...
Malankhulidwe a Pemphero/The language of Prayer 14.08.2023 1:09:23
Masalimo 5:1-12, Abusa a Dallas Goebel afokozera bwino za malankhulidwe a pemphero. Abusa a Dallas alongosora pogwiritsa ntchito Buku la Masalimo chaputa 5. Kufotokoza mwachidule, mayankhulidwe a pemphero ayenera kukhala motere; Pemphero liyenera kukhala ndi cholinga, pemphero liyenera kudzindikira kuti mulungu ndi olungama ndipo amalanga anthu omwe ndi ochimwa, pemphero liyenera kukamba za matemb...
Mulungu achitira chifundo Abrahamu/God shows mercy to Abraham 12.08.2023 59:20
Genesis 16:1-16, Abusa a Dzimbiri afotokoza momveka bwino za chifundo cha mulungu pa anthu ake pamene amulakwira. Buku la Genesis 16 mukupezeka nkhani imene mathero ake akuonetsera kulephera kwa Abrahamu m'banja mwake. Izi zikuoneka pamene mkazi wake akumupangira chiganizo chokwatira mkazi wina kuti amuberekere mwana zomwe zinali zosemphana ndi malonjezo a mulungu. Abrahamu anamvera ndi kulakw...
Mulungu achita ubale ndi munthu/ God enters into a relationship with a man 10.08.2023 49:08
Genesis 15:7-21, Abusa a Hutchens akutitengera mukumvetsetsa gawo lomaliza la chaputa chimenechi cha bukuli. Abusa a Hutchens akukamba za chinthu chokoma chomwe chikupezeka mu nkhaniyi. Mulungu achita ubale ndi munthu. Iye akuchita izi kudzera mupangano limene achita ndi Abrahamu. Pangano limene mathero ake ndi imfa kusanduka cholekanitsa. Mukukambirana komwe kunalipo pakati pa Mulungu ndi Abramu,...
Kukhulupirika kwa Malonjezo a Mulungu/The Faithfulness of God's Promises 07.08.2023 23:13
Genesis 15:1-6, Abusa a Watch akutitengera mukumvetsetsa kwa gawo loyamba la chaputa chimenechi. Abusa a Watch akulongosola bwino lomwe za kudalira ndi kukhulupirira malonjezo a mulungu pogwiritsa ntchito chithunzi cha Abramu mu nkhaniyi. Mulungu wathandiza Abramu kugonjetsa magulu ankhondo ndipo mapeto ake mulungu akuyankhulana ndi Abramu kudzera m'masomphenya. Mulungu akumuuza Abramu kuti as...
Kodi mukutsatira Yesu Khristu?/Are you following Jesus Christ? 28.07.2023 20:37
Abusa a Justin alongosola momveka bwino pogwiritsa ntchito ndime za malemba zosiyanasiaya kulimbikitsa Akhristu kuti apitilize kutsatira Yesu Khristu pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Abusawa agwiritsa ntchito mafunso osiyanasiyana omwe akufunsa onse omwe ndi Akhristu kuti kodi ife timadziwika chiyani ngati akhristu? Popeza tinayitanidwa kukhala okhulupirira ake a Yesu ndi otsatira akenso. Pastor J...
Timapembedza mulungu chifukwa chiyani?/Why do we worship God? 25.07.2023 47:17
Genesis 14:16-24 mu chaputa cha bukuli abusa a Joshua Hutchens afunsa mafunso ophweka kumvetsa koma ovuta kuyankha. Izi achita ndi cholinga chofuna kuthandiza kumvetsetsa ndime ya malemba imeneyi. Mafunso ali motere; Ndi chifukwa chiyani timapembeza mulungu? Ndi chifukwa chiyani timapereka chuma chathu kwa mulungu? Ndi chifukwa chiyani timakhala moyo wa khristu okhulupirika? Yankho la mafunso awa...
Yesu mfumu yozichepetsa/Jesus the humble king 14.07.2023 46:29
Genesis 14:1-16 Bukuli likupitiriza kukhala ulosi komanso nzeru. Mu mavesi amenewa mulungu akutionetsera za mfumu imene ikubwera kudzera mwa Abramu. Abramu apulumutsa Loti monga mfumu ichitira ngakhale sakutionetsera Abramu ngati mfumu. Izi zikulosera za mfumu imene mulungu anayisankha kuti ipulumutse anthu ake kuchokera ku tchimo komanso imfa. Ndipo mfumuyo ndi Yesu Khristu mwana wa mulungu yemwe...
Kukhala moyo osogozedwa ndi mzimu woyera/Living by the spirit 26.06.2023 51:54
Genesis 13:1-18 Abramu wapeza chuma chambiri chimene chikumupanga kukhala munthu wolemera kwambiri. Abramu anabwerera kumalo kumene anamanga tenti komanso guwa lansembe ndipo analambira mulungu. Abramu alambilanso Mulungu kuonetsera kudzipereka kwake kwa mulungu. Abramu ndi Loti anapeza chuma chambiri ndipo ogwira ntchito awo anayamba kukangana. Pamenepo Abramu anathetsa nkangano umenewu popereka...
Kukhala okhadzikika m'malonjezo a Mulungu/Remain firm in God's promises 21.06.2023 37:06
Genesis 12:10-20, pamene njala inagwera dziko la caanani Abramu anapita ku dziko la Igupto. Panalibe ganizo limodzi pakati pake lofuna kubwerera komwe anachokera kuti akapeze chakudya koma anapita ku dziko lowandikana nalo. Ngakhale anatulutsidwa chifukwa cha bodza iye sanalunjike kubwerera kwawo koma anabwerera ku Caanani komwe Mulungu anamuyitanira. Phunziro; Abramu ngakhale anakumana ndi mavuta...
Mbewu ya mzimayi(mwa mkazi wa Abrahamu)/The seed of a Woman(coming through Abraham's wife) 15.06.2023 37:44
Genesis 12:4-8, Mulungu akupitiriza kusunga malonjeza ake omwe anawalengeza kwa Hava atachimwira mulungu. Mulungu akuchititsa mkazi wa Abrahamu yemwe anali chumba kuti akhale ndi mwana. Ndipo kutengera dongosolo la chiyambi cha moyo wa Yesu, abale ake anayambira mwa Abrahamu. Izi zikutilimbikitsa ife monga akhristu kuti tili ndi mulungu amene amasunga malonjezo ake. Mulungu analonjeza moyo wosatha...
Mayitanidwe a Abrahamu/The calling of Abraham 12.06.2023 47:39
Genesis 12:1-3, Mulungu akumuyitana Abrahamu amene akuchokera ku dziko lomwe amapembeza mafano. Mulungu akuyitana Abrahamu yemwe anali opanda kanthu kalikonse pamaso pa mulungu, ndi kuchita naye malonjezo akunthawi zosatha. Abrahamu anakhulupirira mulungu ndi malonjezo ake. Lero ife ngati akhristu kodi takonzeka kusiya ntchito za mum'dima ndi kutsatira mayitanidwe athu omwe mulungu watiyitana...
Pemphero ndi kuthamangira/Prayer and pursuit 31.05.2023 45:02
1 Yohane 5:16,17 mu mpingo, pamene membala wachita tchimo ndi udindo wa abale ndi alongo mu mpingo kuthandiza m'baleyu kuti alape tchimo wachitaro ndi kubwerera kwa mulungu. Komanso pamene tchimo lachitidwa pamaso pa mpingo onse ndi udindo wa mpingo ku pempherera m'bale ameneyu ndi kumuthamangira kuti abwezedwe ndi kuyamba kuyenda m'choonadi. Izi ziyenera kuchitidwa mwa chikondi pofuna...
Yesu Mulungu Ndithu ndi moyo wosatha/Jesus the True God and eternal life 29.05.2023 49:41
1 Yohane 5:18-21 mathero a buku la 1 Yohane angotikumbutsa zonse zomwe zikupezeka mu bukuli. Munthu amene amakonda mulungu samachimwa kawirikawiri. Ana amulungu amaonekera mu ntchito zawo chifukwa mu buku la 1 Yohane mayesero a momwe mungaziwire kuti ndiwe mwana wa mulungu kapena ayi abweresedwa poyera kufuna kutidzindikiritsa. Ndipo kudzera mukudziwa kumeneku timakhala odzadzidwa ndi chidziwitso...
Kuthekera kwa pemphero/Effectiveness of Prayer 26.05.2023 36:04
1 Yohane 5:14-15 pamene talandira chipulumutso timakhala otsimikidzika za moyo wathu wa muyaya umene mulungu analonjeza. Chifukwa cha chitsimikizo chotere timakhulupirira kuti mapemphero athu amayankhidwa ndi mulungu wathu odziwa kuyankha mapemphero athu. Koma kulimba mtima pa moyo wosatha ndi kutsimikizika pa pemphero zimagwira ntchito limodzi. Chifukwa ndi pokhapokha uli ndi kulimba mtima pa moy...
Petro anavomereza za Yesu/Peter's confession of Jesus 23.05.2023 1:02:37
Mateyu 16:5-18 Yesu atafunsa ophunzira ake kuti iwo amati Yesu ndi ndani, Petro anayankha kuti "inu ndi Khristu mwana wa Mulungu wa moyo."Ndipo ulendo wa Petro oyenda ndi Khristu unayambika. Kodi ife ngati akhristu timati Yesu ndi ndani? Nkhristu yemwe ndi opulumutsidwa akuyenera kukwanitsa kuyankha funso limeneli ponena kuti "Yesu ndi Khristu mwana wa mulungu ndi ambuye ndi mpulumu...
Umboni wa Mulungu/God's Testimony 01.05.2023 50:27
1 Yohane 5:6-13 uthenga wabwino omwe Yohane wakhala akulongosola mu buku la 1 Yohane, wakambidwa bwino mu chaputa cha chisanu. Mulungu wa mphamvu zonse akuchitira umboni mwana wake amene ndi Mulungu komanso munthu ndithu. Mulungu atate akuchitira umboni umenewu mu njira zitatu. Njira yoyamba ndi kudzera m'madzi a ubatizo wa Yesu Khristu, magazi a Yesu Khristu pantanda komanso kudzera mzimu. Nj...
Mphatso ya chipulumutso/The gift of salvation 26.04.2023 40:19
2 Petro 1:1-11, aliyense amapatsidwa mphatso ya chipulumutso kudzera mu chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Palibe amapulumutsidwa kudzera mu ntchito zake koma kudzera mu chikhulupiriro chathu mwa Yesu Khristu timapatsidwa mphatso ya chipulumutso. Monga akhristu zinthu zitatu zoyenera kukumbukira,(tapatsidwa Yesu Khristu, tikuyenera kukhala muchikhulupiriro chathu, tikuyenera kuyembekezera chipulumut...
Chikhulupiriro/Faith 18.04.2023 29:28
1 Yohane 5:1-4, chikhulupiriro chimatipanga ife ana ake a mulungu kukhala ofuna kutsatira malamulo ake. Timaona kuti kutsatira malamulo ake ili ngati njira imodzi yomwe ife timaonetsera chikondi chathu pa mulungu wathu. Timaphunzitsa ena potsatira malamulo a mulungu siwolemetsa konse. Ndichikhulupiriro chathu mwa mulungu ndife olimba kuti sitingagwetsedwe konse. 1 John 5:1-4, faith make us childre...
Yesu auka mmanda/Jesus is raised from the tomb 11.04.2023 48:27
Yohane 20:1-18, Yesu anakwanilitsa zonse zomwe anabwerera kuzachita padziko lapansi. Yesu anakwanitsa kulipira ngongole ya machimo yomwe ife sitikanakwanitsa kulipira patokha. Yesu ali m'manda mulungu anamukitsa kwa akufa pakuti iye anali olungama ndipo sanayenera kuti thupi lake lichite chivundi. Tsopano lino ali kumwamba kwa atate ake ndi atate athu, mulungu wake komanso mulungu wathu. Ndiku...
Chikondi chafika pachimake mwa ife/Love is made complete in us 06.04.2023 1:05:06
1 Yohane 4:12-21, onse okhulupirira uthenga wabwino amalumikizidwa ndi mulungu ndipo chiyanjano chawo chimakhala chenicheni. Chifukwa cha chikondi chimenechi ndi chiyanjano chimenechi timaonetsera chikondi chathu pa ena ndipo chikondi chake chimakhala choonadi. Mulungu akutilimbikitsa kufikira tsiku la chiweruzo ndi cholinga chakuti tizayime pamaso pake opanda mulandu koma kupatsidwa mphoto ya moy...
Similar podcasts
Replaio is not a podcast publisher; show names, artwork and audio belong to their authors and are distributed through public RSS feeds.